Olemba- Judgement Katika

Phungu wa dera la ku mpoto cha ku madzulo kwa boma la Salima, Enock Phale wati mkumano wa nyumba ya malamulo unali opindulitsa kwambiri pozindikira kuti nduna komanso aphungu amatha kugawana nzeru moyenerera kudzera mu mkambiraano zomwe ndizopindulira a Malawi.

Enock Phale wayankhula izi lachisanu mu mzinda wa Lilongwe pomwe aphungu amatseka mkumano wa nyumba ya malamulo omwe ndi wa chi nambala 50 omwenso watenga masabata anayi.

Malingana ndi Phale, panali kukhwima kwa ndondomeko zomwe zinaikidwa ndi boma kudzera mu mkambirano ndipo ma bill omwe avomerezeka mnyumbayi athandiza dziko lino potukula ntchito zosiyanasiyana.

“Ma lipoti ochokera mma komiti athandizira a phungu kuzindikira za mayankho omwe angaperekedwe kwa ena mwa mavuto omwe a Malawi akukumana nawo”, Phale anafotokoza motero.

Zina mwa ndondomeko zomwe zakhazikitsikidwa mma unduna monga za umoyo, za mtengatenga, za malonda, za maphunziro, komanso za ulimi zithandiza kutukula umoyo wa a Malawi ambiri.

Ngakhale izi zili chomwechi, anthu akuyenera kukhala ndi chiyembekezo pa zomwe aphungu amakambirana mnyumbayi, pozindikira kuti adindo amakhala ndi kuthera kogwirizana chimodzi kudzera mu mfundo komanso msanamira zosiyanasiyana, ndipo a phungu ambiri kuphatikizira phunguyu anabweretsa anthu osiyanasiyana kulondola adindo awo ku nyumba ya malamulo ndi kudzazionera okha pa mkambirano omwe unalipo mnyumbayi.

By user

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *